Numeri 22:41 - Buku Lopatulika Ndipo kunali kuti m'mawa, Balaki anatenga Balamu, nakwera naye ku misanje ya Baala, ndi kumeneko anaona malekezero a anthuwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali kuti m'mawa, Balaki anatenga Balamu, nakwera naye ku misanje ya Baala, ndi kumeneko anaona malekezero a anthuwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'maŵa mwake Balaki adatenga Balamu, napita naye ku mapiri a Bamoti-Baala, kumene Balamuyo ankatha kuwona mahema onse a Aisraele mpaka ku mathero ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mmawa mwake Balaki anatenga Balaamu napita limodzi ku Bamoti Baala, ndipo kumeneko anakaonako gulu lina la Aisraeliwo. |
namanga misanje ya Baala, kuti apsereze ana ao m'menemo nsembe zopsereza za Baala, chimene sindinawauze, sindinachinene, sichinalowe m'mtima mwanga;
Ndiponso ndidzaletsa mu Mowabu, ati Yehova, iye amene apereka nsembe pamsanje, ndi iye amene afukizira milungu yake.
Popeza moto unatuluka mu Hesiboni, chirangali cha moto m'mzinda wa Sihoni; chatha Ari wa Mowabu, eni misanje ya Arinoni.
Pamenepo Balaki anapha ng'ombe ndi nkhosa, natumizira Balamu, ndi akalonga okhala naye.
Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Ndimangireni kuno maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere kuno ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.
Ndipo Balaki anati naye, Tiyetu, upite nane kumalo kwina, kumene ukawaona; udzaona malekezero ao okha, osawaona onse; ndipo pokhala pamenepo ukanditembererere iwo.
Muononge konse malo onse, amitundu amene mudzawalanda anatumikirako milungu yao, pa mapiri aatali, ndi pa zitunda, ndi pansi pa mitengo yonse yabiriwiri;