Numeri 22:29 - Buku Lopatulika Pamenepo Balamu anati kwa bulu, Chifukwa wandipeputsa; mukadakhala lupanga m'dzanja langa tsopano, ndikadakupha iwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Balamu anati kwa bulu, Chifukwa wandipeputsa; mukadakhala lupanga m'dzanja langa tsopano, ndikadakupha iwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Balamu adauza buluyo kuti, “Chifukwa choti ukuseŵera nane, ndikadakhala ndi lupanga m'manja mwanga, ndikadakupha.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Balaamu anati kwa buluyo, “Wandipusitsa, ndikanakhala ndi lupanga mʼmanja mwanga, ndikanakupha pomwe pano.” |
Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.
Ndipo bulu anati kwa Balamu, Si ndine bulu wako amene umayenda wokwera pa ine chiyambire ndili wako kufikira lero lino? Kodi ndikakuchitira chotere ndi kale lonse? Ndipo anati, Iai.
Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;