Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndimuke kuyambana nao Afilistiwo? Mudzawapereka m'dzanja langa kodi? Ndipo Yehova ananena ndi Davide, Pita, pakuti zoonadi ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako.
Numeri 21:34 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anati kwa Mose, Usamuopa; popeza ndampereka m'manja mwako, iye ndi anthu ake onse, ndi dziko lake; umchitire monga umo unachitira Sihoni mfumu ya Aamori anakhalayo ku Hesiboni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Usamuopa; popeza ndampereka m'manja mwako, iye ndi anthu ake onse, ndi dziko lake; umchitire monga umo unachitira Sihoni mfumu ya Aamori anakhalayo ku Hesiboni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Chauta adauza Mose kuti, “Usamuwope. Ndampereka m'manja mwako pamodzi ndi anthu ake onse ndi dziko lake lomwe. Ndipo umchite zomwe udachita Sihoni mfumu ya Aamori amene ankakhala ku Hesiboni.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anati kwa Mose, “Usachite naye mantha pakuti ndamupereka mʼmanja mwako pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo ndi dziko lake lomwe. Ndipo uchite kwa iye zimene unachita Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamulira ku Hesiboni.” |
Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndimuke kuyambana nao Afilistiwo? Mudzawapereka m'dzanja langa kodi? Ndipo Yehova ananena ndi Davide, Pita, pakuti zoonadi ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako.
Ndipo taonani, mneneri anadza kwa Ahabu mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Kodi waona unyinji uwu waukulu wonse? Taonani, ndidzaupereka m'dzanja mwako lero, kuti udziwe kuti ndine Yehova.
Ndipo munthu uja wa Mulungu anafikako, nalankhula ndi mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Popeza Aaramu amati, Yehova ndiye Mulungu wa kumapiri, osati Mulungu wa kuzigwa, mwa ichi ndidzapereka unyinji uwu waukulu m'dzanja mwako, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.
Pakuti Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.
Chokhachi musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m'dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawachokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.
dzikoli Yehova analikantha pamaso pa gulu la Israele, ndilo dziko la zoweta ndipo anyamata anu ali nazo zoweta.
Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wake, nalimbitsa mtima wake, kuti ampereke m'dzanja lanu, monga lero lino.
nati nao, Tamverani, Israele, muyandikiza kunkhondo lero pa adani anu; musafumuka mitima yanu; musachita mantha, kapena kunjenjemera, kapena kuopsedwa pamaso pao;
Pamenepo tinatembenuka, ndi kubwera kunka njira ya ku Basani; ndipo Ogi mfumu ya Basani anatuluka kukomana nafe, kumenyana nafe nkhondo, iye ndi anthu ake onse, ku Ederei.
(Pakuti Ogi mfumu ya Basani anatsala yekha wa iwo otsalira Arefaimu; taonani, kama wake ndiye kama wachitsulo; sukhala kodi mu Raba wa ana a Amoni? Utali wake mikono isanu ndi inai, kupingasa kwake mikono inai, kuyesa mkono wa munthu).
Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamachita mantha, kapena kuopsedwa chifukwa cha iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; Iye sadzakusowani, kapena kukusiyani.
Musamawaopa; mukumbukire bwino chimene Yehova Mulungu wanu anachitira Farao, ndi Ejipito wonse;
Musamaopa pamaso pao; popeza Yehova Mulungu wanu ali pakati pa inu, Mulungu wamkulu ndi woopsa.
Adzaperekanso mafumu ao m'dzanja mwanu, ndipo muwafafanize maina ao pansi pa thambo; palibe munthu mmodzi adzaima pamaso panu, kufikira mutawaononga.
Pamenepo Yoswa ananena nao, Musaope, musatenge nkhawa; khalani amphamvu, nimulimbike mtima; pakuti Yehova adzatero ndi adani anu onse amene mugwirana nao nkhondo.
Ndipo Yehova ananena ndi Yoswa, Usawaope, pakuti ndawapereka m'dzanja lako; palibe mmodzi wa iwo adzaima pamaso pako.
pamenepo muziuka m'molalira ndi kulowa m'mzinda; pakuti Yehova Mulungu wanu; adzaupereka m'manja mwanu.
Ndipo Yefita anawindira Yehova chowinda, nati, Mukaperekatu ana a Amoni m'dzanja langa,
Tsono Davide anafunsiranso kwa Yehova. Ndipo Yehova anamyankha iye, nati, Nyamuka, nutsikire ku Keila; pakuti ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako.