Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 10:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo Yehova ananena ndi Yoswa, Usawaope, pakuti ndawapereka m'dzanja lako; palibe mmodzi wa iwo adzaima pamaso pako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo Yehova ananena ndi Yoswa, Usawaope, pakuti ndawapereka m'dzanja lako; palibe mmodzi wa iwo adzaima pamaso pako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Ndipo Chauta adauza Yoswa kuti, “Usaŵaope anthu amenewo. Ndaŵapereka kale kwa iwe kuti uŵagonjetse. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene adzatha kulimbika.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Yehova anati kwa Yoswa, “Usawaope, Ine ndawapereka mʼdzanja lako. Palibe ndi mmodzi mwa amenewa amene adzalimbe.”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 10:8
16 Mawu Ofanana  

Ndipo taonani, mneneri anadza kwa Ahabu mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Kodi waona unyinji uwu waukulu wonse? Taonani, ndidzaupereka m'dzanja mwako lero, kuti udziwe kuti ndine Yehova.


Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?


Ndipo Yehova anati kwa ine, Usamuopa; popeza ndampereka iye ndi anthu ake onse, ndi dziko lake, m'dzanja lako; umchitire monga umo unachitira Sihoni mfumu ya Aamori, amene anakhala mu Hesiboni.


Adzaperekanso mafumu ao m'dzanja mwanu, ndipo muwafafanize maina ao pansi pa thambo; palibe munthu mmodzi adzaima pamaso panu, kufikira mutawaononga.


Pamenepo Yoswa ananena nao, Musaope, musatenge nkhawa; khalani amphamvu, nimulimbike mtima; pakuti Yehova adzatero ndi adani anu onse amene mugwirana nao nkhondo.


Ndipo Yoswa anawadzidzimukitsa; popeza anakwera kuchokera ku Giligala usiku wonse.


Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope chifukwa cha iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israele; udzawadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agaleta ao ndi moto.


Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Usaope, kapena kutenga nkhawa, tenga anthu onse a nkhondo apite nawe, ndipo tauka, kwera ku Ai; taona, ndapereka m'dzanja lako mfumu ya ku Ai, ndi anthu ake ndi mzinda wake ndi dziko lake;


Ndipo Yehova ananena naye, Popeza Ine ndidzakhala nawe udzakantha Amidiyani ngati munthu mmodzi.


Ndipo kunali usiku womwewo, kuti Yehova ananena naye, Tauka, tatsikira kumisasa; pakuti ndaipereka m'dzanja lako.


Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo, ndipo Iye adzakuperekani inu m'manja athu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa