Khosi lako likunga nsanja yaminyanga; maso ako akunga matawale a ku Hesiboni, a pa chipata cha Batirabimu; mphuno yako ikunga nsanja ya ku Lebanoni imene iloza ku Damasiko.
Numeri 21:26 - Buku Lopatulika Popeza Hesiboni ndiwo mzinda wa Sihoni mfumu ya Aamori, imene idathira nkhondo pa mfumu idafayo ya Mowabu, nilanda dziko lake m'dzanja lake kufikira Arinoni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Popeza Hesiboni ndiwo mudzi wa Sihoni mfumu ya Aamori, imene idathira nkhondo pa mfumu idafayo ya Mowabu, nilanda dziko lake m'dzanja lake kufikira Arinoni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Hesiboni unali mzinda wa Sihoni mfumu ya Aamori, amene adaamenyana ndi mfumu yakale ya Amowabu, ndipo adamlanda dziko lake lonse mpaka ku mtsinje wa Arinoni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Hesiboni unali mzinda wa Sihoni mfumu ya Aamori, yemwe anamenyana ndi mfumu yakale ya dziko la Mowabu. Lonselo linakhala dziko lake mpaka ku Arinoni. |
Khosi lako likunga nsanja yaminyanga; maso ako akunga matawale a ku Hesiboni, a pa chipata cha Batirabimu; mphuno yako ikunga nsanja ya ku Lebanoni imene iloza ku Damasiko.
Mutu wako ukunga Karimele, ndi tsitsi la pamutu pako likunga nsalu yofiirira; mfumu yamangidwa ndi nkhata zake ngati wam'nsinga.
Palibenso kutamanda Mowabu; mu Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu wa anthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe.
Mowabu wachitidwa manyazi, pakuti wathyoka; kuwa nulire, nunene mu Arinoni, kuti Mowabu wapasuka.
Iwo amene anathawa aima opanda mphamvu pansi pamthunzi wa Hesiboni; pakuti moto watuluka mu Hesiboni, ndi malawi a moto m'kati mwa Sihoni, nadya ngodya ya Mowabu, ndi pakati pamutu pa ana a phokoso.
Ndipo Israele analanda mizinda iyi yonse; nakhala Israele m'mizinda yonse ya Aamori; mu Hesiboni ndi midzi yake yonse.
Chifukwa chake iwo akunena mophiphiritsa akuti, Idzani ku Hesiboni, mzinda wa Sihoni umangike, nukhazikike.
atakantha Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala mu Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basani, wakukhala mu Asitaroti, ku Ederei.
Malire ao anayambira ku Aroere wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mzinda uli pakati pa chigwa ndi chidikha chonse cha ku Medeba;
Hesiboni ndi mizinda yake yonse yokhala pachidikha; Diboni, ndi Bamoti-Baala ndi Bete-Baala-Meoni;
Ndipo malire ao ndiwo Yazere, ndi mizinda yonse ya Giliyadi, ndi dziko la ana a Amoni logawika pakati, mpaka ku Aroere, wokhala chakuno cha Raba;
Pokhala Israele mu Hesiboni ndi midzi yake, ndi mu Aroere ndi midzi yake ndi m'mizinda yonse yokhala m'mphepete mwa Arinoni zaka mazana atatu; munalekeranji kulandanso nthawi ija?