Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 48:2 - Buku Lopatulika

2 Palibenso kutamanda Mowabu; mu Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu wa anthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Palibenso kutamanda Mowabu; m'Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu wa anthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Mowabu sakutchukanso. Adampanganirana zachiwembu ku Hesiboni, adati, ‘Tiyeni timuwononge, asakhalenso mtundu wa anthu.’ Ndipo inu okhala ku Madimeni, adzakukhalitsani chete, adzakupirikitsani ndi lupanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Palibenso amene akutamanda Mowabu; ku Hesiboni anthu anamupanganira zoyipa: ‘Bwerani, tiyeni timuwonongeretu kuti asakhalenso mtundu wa anthu.’ Inunso anthu a ku Madimena, adzakukhalitsani chete; ankhondo adzakupirikitsani.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 48:2
20 Mawu Ofanana  

Katundu wa Mowabu. Pakuti usiku umodzi Ari wa ku Mowabu wapasuka, nakhala chabe; usiku umodzi Kiri wa Mowabu wapasuka, nakhala chabe.


Mtima wanga ufuula chifukwa cha Mowabu: akulu ake athawira ku Zowari, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa chikweza cha Luhiti akwera alikulira, pakuti m'njira ya Horonaimu akweza mfuu wa chionongeko.


Koma tsopano Yehova wanena, nati, Zisanapite zaka zitatu monga zaka za wolembedwa ntchito, ulemerero wa Mowabu udzakhala wonyozeka, ndi khamu lalikulu lake, ndi otsala adzakhala ang'onong'ono ndi achabe.


Chifukwa m'phiri limeneli dzanja la Yehova lidzakhalamo, ndipo Mowabu adzaponderezedwa pansi m'malo ake, monga udzu uponderezedwa padzala.


Pakuti Yehova, Mulungu wa Israele, atero kwa ine, Tenga chikho cha vinyo wa ukaliwu padzanja langa, ndi kumwetsa mitundu yonse, imene ndikutumizirako.


Ndipo ndinatenga chikho padzanja la Yehova, ndinamwetsa mitundu yonse, imene Yehova ananditumizirako;


Ngati malembawa achoka pamaso panga, ati Yehova, pamenepo mbeunso ya Israele idzaleka kukhala mtundu pamaso panga kunthawi zonse.


Kodi sulingalira chomwe anena anthu awa, kuti, Mabanja awiri amene Yehova anawasankha, wataya iwo? Chomwecho anyoza anthu anga, kuti asakhalenso mtundu pamaso pao.


Usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; pakuti Ine ndili ndi iwe; pakuti Ine ndidzathetsa mitundu yonse kumene ndinakuingitsirako iwe, koma sindidzakuthetsa iwe; koma ndidzakulangiza ndi chiweruziro, ndipo sindidzakusiya konse wosalangidwa.


Inu nonse akumzungulira, mumchitire iye chisoni, inu nonse akudziwa dzina lake; muti, Chibonga cholimba chathyokatu, ndodo yokoma!


Ndipo Mowabu adzaonongeka asakhalenso mtundu wa anthu, chifukwa anadzikuzira yekha pa Yehova.


Iwo amene anathawa aima opanda mphamvu pansi pamthunzi wa Hesiboni; pakuti moto watuluka mu Hesiboni, ndi malawi a moto m'kati mwa Sihoni, nadya ngodya ya Mowabu, ndi pakati pamutu pa ana a phokoso.


Kuwa, iwe Hesiboni, pakuti Ai wapasuka; lirani, inu ana aakazi a Raba, muvale chiguduli; chitani maliro, thamangani kwina ndi kwina pamipanda; pakuti mfumu yao idzalowa m'ndende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi.


Ndipo ndidzachititsa Elamu mantha pamaso pa amaliwongo ao, ndi pamaso pa iwo ofuna moyo wao; ndipo ndidzatengera choipa pa iwo, mkwiyo wanga waukali, ati Yehova; ndipo ndidzatumiza lupanga liwalondole, mpaka nditawatha;


Ndipo ana a Rubeni anamanga Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Kiriyataimu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa