Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 48:3 - Buku Lopatulika

3 Mau amveka kuchokera ku Horonaimu, kufunkha ndi kuononga kwakukulu!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Mau amveka kuchokera ku Horonaimu, kufunkha ndi kuononga kwakukulu!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 “Imvani kulira kwachisoni kwa anthu a ku Horonaimu, akuti, ‘Chisakazo ndi chiwonongeko chachikulutu!’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Tamvani mfuwu wa anthu a ku Horonaimu. Iwo akulira kuti, ‘Kusakazika ndi kuwonongeka kwakukulu.’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 48:3
12 Mawu Ofanana  

Akwera ku Kachisi, ndi ku Diboni, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Mowabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndevu zonse zametedwa.


Mtima wanga ufuula chifukwa cha Mowabu: akulu ake athawira ku Zowari, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa chikweza cha Luhiti akwera alikulira, pakuti m'njira ya Horonaimu akweza mfuu wa chionongeko.


Pakuti kulira kwamveka kuzungulira malire a Mowabu; kukuwa kwake kwafikira ku Egilaimu, ndi kukuwa kwake kwafikira ku Beerelimu.


Chomwecho ndinati, Usandiyang'ane ine, ndilira ndi kuwawa mtima; usafulumire kunditonthoza ine, chifukwa cha kufunkhidwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.


Munthuyo akhale ngati mizinda imene Yehova anapasula, osalekerera; amve mfuu mamawa, ndi mkuwo pausana;


Yehova atero: Taonani, madzi adzakwera kutuluka kumpoto, nadzakhala mtsinje wosefuka, nadzasefukira padziko ndi pa zonse zili m'mwemo, pamzinda ndi pa onse okhalamo; ndipo amuna adzalira, ndi onse okhala m'dziko adzakuwa.


Kuyambira kufuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleyale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zowari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pamadzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja.


Mowabu waonongedwa; ang'ono ake amveketsa kulira.


Pakuti adzakwera pa chikweza cha Luhiti ndi kulira kosaleka; pakuti pa chitsiko cha Horonaimu amva kulira kowawa kwa chionongeko.


Mau akufuula ochokera ku Babiloni, ndi a chionongeko chachikulu ku dziko la Ababiloni!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa