Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 48:1 - Buku Lopatulika

1 Za Mowabu. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Tsoka Nebo! Pakuti wapasuka; Kiriyataimu wachitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lachitidwa manyazi lapasudwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Za Mowabu. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Tsoka Nebo! Pakuti wapasuka; Kiriyataimu wachitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lachitidwa manyazi lapasudwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ponena za Mowabu, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, “Tsoka kwa mzinda wa Nebo, wasanduka chipululu. Kiriyataimu wachititsidwa manyazi, wagonjetsedwa. Linga lake lankhondo alinyoza ndipo aligumula.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ponena za Mowabu: Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Tsoka kwa mzinda wa Nebo, chifukwa wawonongedwa. Mzinda wa Kiriyataimu wachititsidwa manyazi ndipo wagonjetsedwa; linga lichititsidwa manyazi ndipo lagumulidwa.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 48:1
19 Mawu Ofanana  

Chaka chakhumi ndi chinai ndipo anadza Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, nawakantha Arefaimu mu Asiteroti-Karanaimu, ndi Azuzimu mu Hamu, ndi Aemimu mu Savekiriyataimu,


Woyamba ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake. Mowabu; yemweyo ndi atate wa Amowabu kufikira lero.


Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Mowabu, ndi a kuphiri la Seiri, amene simunalole Israele awalowere, pakutuluka iwo m'dziko la Ejipito, koma anawapatukira osawaononga;


Chifukwa m'phiri limeneli dzanja la Yehova lidzakhalamo, ndipo Mowabu adzaponderezedwa pansi m'malo ake, monga udzu uponderezedwa padzala.


Ndipo linga la pamsanje la machemba ako Iye waligwetsa, naligonetsa pansi, nalifikitsa padothi, ngakhale pafumbi.


Ine Yehova ndiusunga uwo; ndidzauthirira madzi nthawi zonse; ndidzausunga usiku ndi usana, kuti angauipse.


Edomu, ndi Mowabu, ndi ana a Amoni,


nuzitumize kwa mfumu ya Edomu, ndi kwa mfumu ya Mowabu, ndi kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kwa mfumu ya Tiro, ndi kwa mfumu ya Sidoni, ndi dzanja la amithenga amene afika ku Yerusalemu kwa Zedekiya mfumu ya Yuda;


Ejipito, ndi Yuda, ndi Edomu, ndi ana a Amoni, ndi a Mowabu, ndi onse ometa m'mphepete mwa tsitsi lao, okhala m'chipululu; pakuti amitundu onse ali osadulidwa, ndi nyumba ya Israele ili yosadulidwa m'mtima.


Ndimuona, koma tsopano ai; ndimpenya, koma si pafupi ai; idzatuluka nyenyezi mu Yakobo, ndi ndodo yachifumu idzauka mu Israele, nidzakantha malire a Mowabu, nidzapasula ana onse a Seti.


Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazere, ndi Nimira, ndi Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Sibima, ndi Nebo, ndi Beoni,


Nachokera ku Alimoni-Dibulataimu, nayenda namanga m'mapiri a Abarimu, chakuno cha Nebo.


ndi Kiriyataimu, ndi Sibima, ndi Zeretisahara, m'phiri la kuchigwa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa