Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 21:25 - Buku Lopatulika

25 Ndipo Israele analanda mizinda iyi yonse; nakhala Israele m'mizinda yonse ya Aamori; mu Hesiboni ndi midzi yake yonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo Israele analanda midzi iyi yonse; nakhala Israele m'midzi yonse ya Aamori; m'Hesiboni ndi milaga yake yonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Aisraele adalanda mizinda yonseyi nakhala m'mizinda yonse ya Aamori, ku Hesiboni ndi m'midzi yake yonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Ndipo Aisraeli analanda mizinda yonse ya Aamori, nakhalamo kuphatikizapo Hesiboni ndi midzi yake yozungulira.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 21:25
17 Mawu Ofanana  

Khosi lako likunga nsanja yaminyanga; maso ako akunga matawale a ku Hesiboni, a pa chipata cha Batirabimu; mphuno yako ikunga nsanja ya ku Lebanoni imene iloza ku Damasiko.


Ndi Hesiboni afuula zolimba, ndi Eleyale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; chifukwa chake amuna ankhondo a Mowabu afuula zolimba; moyo wake wanthunthumira m'kati mwake.


Palibenso kutamanda Mowabu; mu Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu wa anthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe.


Kuyambira kufuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleyale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zowari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pamadzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja.


Iwo amene anathawa aima opanda mphamvu pansi pamthunzi wa Hesiboni; pakuti moto watuluka mu Hesiboni, ndi malawi a moto m'kati mwa Sihoni, nadya ngodya ya Mowabu, ndi pakati pamutu pa ana a phokoso.


Ndi mkulu wako ndiye Samariya, wokhala kudzanja lako lamanzere, iye ndi ana ake aakazi; ndi mng'ono wako wokhala kudzanja lako lamanja ndiye Sodomu ndi ana ake aakazi.


Taona, mphulupulu ya mng'ono wako Sodomu ndi iye, kudzikuza, kuchuluka kwa chakudya, ndi kupumula kwa mtambasali, anali nako iye ndi ana ake; ndipo sanalimbitse dzanja la wosauka ndi wosowa.


Ndipo ndidzabweza undende wao, undende wa Sodomu ndi ana ake, ndi undende wa Samariya ndi ana ake, ndi undende wa andende ako pakati pao;


Ndipo ndinakukwezani kuchokera m'dziko la Ejipito, ndi kukutsogolerani zaka makumi anai m'chipululu, kuti mulandire dziko la Aamori likhale cholowa chanu.


Popeza Hesiboni ndiwo mzinda wa Sihoni mfumu ya Aamori, imene idathira nkhondo pa mfumu idafayo ya Mowabu, nilanda dziko lake m'dzanja lake kufikira Arinoni.


Chomwecho Israele anakhala m'dziko la Aamori.


Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazere, ndi Nimira, ndi Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Sibima, ndi Nebo, ndi Beoni,


Ndipo Ahori anakhala mu Seiri kale, koma ana a Esau analanda dziko lao, nawaononga pamaso pao, nakhala m'malo mwao; monga Israele anachitira dziko lakelake, limene Yehova anampatsa).


Pamenepo ndinakulowetsani inu m'dziko la Aamori okhala tsidya lija la Yordani; nagwirana nanu iwowa; ndipo ndinawapereka m'dzanja lanu, nimunalandira dziko lao likhale lanulanu; ndipo ndinawaononga pamaso panu.


Pokhala Israele mu Hesiboni ndi midzi yake, ndi mu Aroere ndi midzi yake ndi m'mizinda yonse yokhala m'mphepete mwa Arinoni zaka mazana atatu; munalekeranji kulandanso nthawi ija?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa