Numeri 21:20 - Buku Lopatulika atachoka ku Bamoti ku chigwa chili m'dziko la Mowabu, ku mutu wa Pisiga, popenyana ndi chipululu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 atachoka ku Bamoti ku chigwa chili m'dziko la Mowabu, ku mutu wa Pisiga, popenyana ndi chipululu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kuchokera ku Bamoti adafika ku chigwa cha m'dziko la Mowabu, kudzera njira ya pamwamba pa phiri la Pisiga, loyang'anana ndi chipululu cham'munsi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo atachoka ku Bamoti anapita ku chigwa cha dziko la Mowabu kudzera njira ya pamwamba pa phiri la Pisiga, moyangʼanana ndi Yesimoni. |
Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, namanga mahema m'zigwa za Mowabu, tsidya la Yordani ku Yeriko.
Ndipo anamuka naye ku thengo la Zofimu, pamwamba pa Pisiga, namangako maguwa a nsembe asanu ndi awiri, napereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo paguwa la nsembe lililonse.
Iwo ndiwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eleazara wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'zidikha za Mowabu ku Yordani pafupi pa Yeriko.
Tsidya lija la Yordani, m'dziko la Mowabu, Mose anayamba kufotokozera chilamulo ichi, ndi kuti,
Kwera kumwamba ku Pisiga, nukweze maso ako kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera, ndi kum'mawa, nuyang'ane ndi maso ako; popeza sudzaoloka Yordani uyo.
Ndipo Mose anakwera kuchokera ku zidikha za Mowabu, kunka kuphiri la Nebo, pamwamba pa Pisiga, popenyana ndi Yeriko. Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse la Giliyadi, kufikira ku Dani;
ndi chidikha chonse tsidya lija la Yordani kum'mawa, kufikira ku Nyanja ya Araba, pa tsinde lake la Pisiga.