Pakuti ana aakazi a Mowabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati chisa chofwanchuka.
Numeri 21:13 - Buku Lopatulika Atachokako anayenda ulendo, namanga mahema tsidya lina la Arinoni, wokhala m'chipululu, wogwera ku malire a Aamori; popeza Arinoni ndiwo malire a Mowabu, pakati pa Mowabu ndi Aamori. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Atachokako anayenda ulendo, namanga mahema tsidya lina la Arinoni, wokhala m'chipululu, wogwera ku malire a Aamori; popeza Arinoni ndiwo malire a Mowabu, pakati pa Mowabu ndi Aamori. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kuchokera kumeneko adakamanga patsidya pa mtsinje wa Arinoni umene uli m'chipululu chochokera ku malire a dziko la Amori. Mtsinje wa Arinoni umene ndiwo malire a Mowabu, uli pakati pa dziko la Mowabu ndi dziko la Amori. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anasamukanso kumeneko nakamanga moyandikana ndi Arinoni mʼdera limene lili mʼchipululu chimene chimafika mʼdziko la Aamori. Arinoni ndiwo malire a Mowabu ndi Aamori. |
Pakuti ana aakazi a Mowabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati chisa chofwanchuka.
Mowabu wachitidwa manyazi, pakuti wathyoka; kuwa nulire, nunene mu Arinoni, kuti Mowabu wapasuka.
Chifukwa chake, ananena m'buku la Nkhondo za Yehova, Waheba mu Sufa, ndi miyendo ya Arinoni;
Pamene Balaki anamva kuti wafika Balamu, anamtulukira kukakomana naye kumzinda wa Mowabu, wokhala m'mphepete mwa Arinoni, ndiwo ku malekezero a malire ake.
Uka, yenda ulendo wako, ndi kuoloka mtsinje wa Arinoni; taonani, ndapereka Sihoni mfumu ya Hesiboni, Mwamori, ndi dziko lake m'dzanja lako; yamba kulilandira, ndi kuutsana naye nkhondo.
Pamenepo anayenda m'chipululu, naphazira dziko la Edomu, ndi dziko la Mowabu, nadzera kum'mawa kwa dziko la Mowabu, namanga misasa tsidya lija la Arinoni; osalowa malire a Mowabu, pakuti Arinoni ndi malire a Mowabu.