Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 21:14 - Buku Lopatulika

14 Chifukwa chake, ananena m'buku la Nkhondo za Yehova, Waheba mu Sufa, ndi miyendo ya Arinoni;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Chifukwa chake, ananena m'buku la Nkhondo za Yehova, Waheba m'Sufa, ndi miyendo ya Arinoni;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Nchifukwa chake buku la nkhondo za Chauta limanena kuti, “Mzinda wa Waheba uli ku Sufa, ku zigwa za Arinoni,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Nʼchifukwa chake Buku la Nkhondo za Yehova limati, “Mzinda wa Wahebu uli mu Sufa, mu zigwa za Arinoni,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 21:14
8 Mawu Ofanana  

nawauza aphunzitse ana Ayuda nyimbo iyi ya Uta, onani inalembedwa m'buku la Yasara,


Pakuti ana aakazi a Mowabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati chisa chofwanchuka.


Atachokako anayenda ulendo, namanga mahema tsidya lina la Arinoni, wokhala m'chipululu, wogwera ku malire a Aamori; popeza Arinoni ndiwo malire a Mowabu, pakati pa Mowabu ndi Aamori.


ndi zigwa za miyendoyo zakutsikira kwao kwa Ari, ndi kuyandikizana ndi malire a Mowabu.


Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse nawatanthauzira iwo m'malembo onse zinthu za Iye yekha.


Uka, yenda ulendo wako, ndi kuoloka mtsinje wa Arinoni; taonani, ndapereka Sihoni mfumu ya Hesiboni, Mwamori, ndi dziko lake m'dzanja lako; yamba kulilandira, ndi kuutsana naye nkhondo.


Ndipo dzuwa linalinda, ndi mwezi unaima mpaka anthu adabwezera chilango adani ao. Kodi ichi sichilembedwa m'buku la Yasara? Ndipo dzuwa linakhala pakati pa thambo, losafulumira kulowa ngati tsiku lamphumphu.


Ndipo Saulo anati kwa Davide, Ona, mwana wanga wamkazi wamkulu, dzina lake Merabi, iyeyo ndidzakupatsa akhale mkazi wako; koma undikhalire ngwazi, nuponye nkhondo za Yehova. Pakuti Saulo anati, Dzanja langa lisamkhudze, koma dzanja la Afilisti ndilo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa