Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 21:13 - Buku Lopatulika

13 Atachokako anayenda ulendo, namanga mahema tsidya lina la Arinoni, wokhala m'chipululu, wogwera ku malire a Aamori; popeza Arinoni ndiwo malire a Mowabu, pakati pa Mowabu ndi Aamori.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Atachokako anayenda ulendo, namanga mahema tsidya lina la Arinoni, wokhala m'chipululu, wogwera ku malire a Aamori; popeza Arinoni ndiwo malire a Mowabu, pakati pa Mowabu ndi Aamori.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Kuchokera kumeneko adakamanga patsidya pa mtsinje wa Arinoni umene uli m'chipululu chochokera ku malire a dziko la Amori. Mtsinje wa Arinoni umene ndiwo malire a Mowabu, uli pakati pa dziko la Mowabu ndi dziko la Amori.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Anasamukanso kumeneko nakamanga moyandikana ndi Arinoni mʼdera limene lili mʼchipululu chimene chimafika mʼdziko la Aamori. Arinoni ndiwo malire a Mowabu ndi Aamori.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 21:13
8 Mawu Ofanana  

Pakuti ana aakazi a Mowabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati chisa chofwanchuka.


Mowabu wachitidwa manyazi, pakuti wathyoka; kuwa nulire, nunene mu Arinoni, kuti Mowabu wapasuka.


Chifukwa chake, ananena m'buku la Nkhondo za Yehova, Waheba mu Sufa, ndi miyendo ya Arinoni;


Pamene Balaki anamva kuti wafika Balamu, anamtulukira kukakomana naye kumzinda wa Mowabu, wokhala m'mphepete mwa Arinoni, ndiwo ku malekezero a malire ake.


Ukani tsopano, olokani mtsinje wa Zeredi. Ndipo tinaoloka mtsinje wa Zeredi.


Lero lomwe utumphe malire a Mowabu, ndiwo Ari.


Uka, yenda ulendo wako, ndi kuoloka mtsinje wa Arinoni; taonani, ndapereka Sihoni mfumu ya Hesiboni, Mwamori, ndi dziko lake m'dzanja lako; yamba kulilandira, ndi kuutsana naye nkhondo.


Pamenepo anayenda m'chipululu, naphazira dziko la Edomu, ndi dziko la Mowabu, nadzera kum'mawa kwa dziko la Mowabu, namanga misasa tsidya lija la Arinoni; osalowa malire a Mowabu, pakuti Arinoni ndi malire a Mowabu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa