Numeri 2:25 - Buku Lopatulika Mbendera ya chigono cha Dani izikhala kumpoto monga mwa makamu ao; ndi kalonga wa ana a Dani ndiye Ahiyezere mwana wa Amisadai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mbendera ya chigono cha Dani izikhala kumpoto monga mwa makamu ao; ndi kalonga wa ana a Dani ndiye Ahiyezere mwana wa Amisadai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Mbali yakumpoto kuzikhala mbendera ya zithando za fuko la Dani, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Danilo ndi Ahiyezere mwana wa Amishadai, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kumpoto kudzakhala msasa wa magulu a Dani pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Adani ndi Ahiyezeri mwana wa Amisadai. |
A ana a Dani, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Pamenepo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Ahiyezere mwana wa Amisadai.
Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.
Ndi kalonga wa nyumba ya makolo ya mabanja la Merari ndiye Zuriyele mwana wa Abihaili; azimanga mahema ao pa mbali ya chihema cha kumpoto.
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Ahiyezere mwana wa Amisadai.