Ndipo anyamata a Isaki anakumba m'chigwa, napeza kumeneko chitsime cha madzi otumphuka.
Numeri 19:17 - Buku Lopatulika Ndipo atengereko wodetsedwayo mapulusa akupsererawo a nsembe yauchimo, nathirepo m'chotengera madzi oyenda; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo atengereko wodetsedwayo mapulusa akupsererawo a nsembe yauchimo, nathirepo m'chotengera madzi oyenda; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Woipitsidwayo amtengereko m'mbiya phulusa la nsembe yopsereza yopepesera machimo, ndipo aonjezemo madzi abwino atsikulo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Za munthu wodetsedwayo: ikani phulusa lochokera ku nsembe ya chiyeretso mu mtsuko ndi kuthiramo madzi abwino. |
Ndipo anyamata a Isaki anakumba m'chigwa, napeza kumeneko chitsime cha madzi otumphuka.
Ndiwe kasupe wa m'minda, chitsime cha madzi amoyo, ndi mitsinje yoyenda yochokera ku Lebanoni.
Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.
Tsiku lomwelo padzatsegukira nyumba ya Davide ndi okhala mu Yerusalemu kasupe wa kwa uchimo ndi chidetso.
ndi munthu woyera atenge hisope, namviike m'madzimo, ndi kuwawaza pahema ndi pa zotengera zonse, ndi pa anthu anali pomwepo, ndi pa iye wakukhudza fupa, kapena wophedwa, kapena wakufa, kapena manda.
Ndipo munthu woyera aole mapulusa a ng'ombe yaikaziyo, nawaike kunja kwa chigono, m'malo moyera: ndipo awasungire khamu la ana a Israele akhale a madzi akusiyanitsa; ndiwo nsembe yauchimo.
zonse zakulola moto, mupititse m'moto, ndipo zidzakhala zoyera; koma muziyeretsenso ndi madzi akusiyanitsa. Koma zonse zosalola moto, muzipititse m'madzi.
Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka m'kati mwake.
Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi ng'ombe zamphongo, ndi makala a ng'ombe yamthandi owazawaza pa iwo odetsedwa, upatutsa kufikira chiyeretso cha thupi;
chifukwa Mwanawankhosa wakukhala pakati pa mpando wachifumu adzawaweta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pao.