Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 7:38 - Buku Lopatulika

38 Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka m'kati mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka m'kati mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Paja Malembo akuti, ‘Munthu wokhulupirira Ine, mtima wake udzakhala ngati gwelo la mitsinje ya madzi opatsa moyo.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Malemba kuti ‘Aliyense amene akhulupirira Ine, mitsinje yamadzi amoyo idzatuluka kuchokera mʼkati mwake.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 7:38
16 Mawu Ofanana  

M'kamwa mwa wolungama ndi kasupe wa moyo; koma m'kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.


Mau a m'kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya; kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wodzala.


Chifukwa chake mudzakondwera pakutunga madzi m'zitsime za chipulumutso.


Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba; pakuti m'chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m'dziko loti see.


Pakuti ndidzathira madzi padziko limene lilibe madzi, ndi mitsinje pa nthaka youma; ndidzathira mzimu wanga pa mbeu yako, ndi mdalitso wanga pa obadwa ako;


Inu nonse, inu akumva ludzu, idzani kumadzi; ndi osowa ndalama idzani inu mugule mudye; inde idzani, mugule vinyo ndi mkaka opanda ndalama ndi opanda mtengo wake.


ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'chilala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ake saphwa konse.


Ndipo kunena za Ine, ili ndi pangano langa ndi iwo, ati Yehova; mzimu wanga umene uli pa iwe, ndi mau anga amene ndaika m'kamwa mwako sadzachoka m'kamwa mwako, pena m'kamwa mwa ana ako, pena m'kamwa mwa mbeu ya mbeu yako, ati Yehova, kuyambira tsopano ndi kunthawi zonse.


Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo kuti madzi amoyo adzatuluka ku Yerusalemu; gawo lao lina kunka ku nyanja ya kum'mawa, ndi gawo lina kunka ku nyanja ya kumadzulo; adzatero nyengo ya dzinja ndi ya mwamvu.


Yesu anayankha nati kwa iye, Ukadadziwa mtulo wa Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse Ine ndimwe; ukadapempha Iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo.


koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira kumoyo wosatha.


pakuti chipatso cha kuunika tichipeza mu ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi choonadi,


Yehova Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri wa pakati panu, wa abale anu, wonga ine; muzimvera iye;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa