Numeri 31:23 - Buku Lopatulika23 zonse zakulola moto, mupititse m'moto, ndipo zidzakhala zoyera; koma muziyeretsenso ndi madzi akusiyanitsa. Koma zonse zosalola moto, muzipititse m'madzi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201423 zonse zakulola moto, mupititse m'moto, ndipo zidzakhala zoyera; koma muziyeretsenso ndi madzi akusiyanitsa. Koma zonse zosalola moto, muzipititse m'madzi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa23 zonse zimene sizingathe kupsa ndi moto, muziike pa moto, ndipo zidzayeretsedwa. Komabe ziyeretsedwenso ndi madzi oyeretsera, ndipo chilichonse chimene chingathe kupsa ndi moto, muchiviike m'madzi omwewo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero23 ndi china chilichonse chimene sichingapse ndi moto muchidutsitse pa moto, ndipo chidzayeretsedwa. Komanso chiyeretsedwe ndi madzi oyeretsa. Ndipo chilichonse chimene chingapse ndi moto muchidutsitse mʼmadzimo. Onani mutuwo |
Ndipo chilichonse chakufa cha izi chikagwera kanthu, kanthuka kadzakhala kodetsedwa; ngakhale chipangizo chamtengo, kapena chovala, kapena chikopa kapena thumba, chipangizo chilichonse chimene agwira nacho ntchito, achiviike m'madzi, ndipo chidzakhala chodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo chidzakhala choyera.