Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 19:10 - Buku Lopatulika

Ndipo wakuola mapulusayo a ng'ombe yaikazi atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo likhale lemba losatha kwa ana a Israele, ndi kwa mlendo wakukhala pakati pao.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo wakuola mapulusayo a ng'ombe yaikazi atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo likhale lemba losatha kwa ana a Israele, ndi kwa mlendo wakukhala pakati pao.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Munthu amene aola phulusa la ng'ombe achape zovala, koma iyenso adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Limeneli likhale lamulo lamuyaya kwa Aisraele ndi kwa mlendo wokhala pakati pao.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Munthu wochotsa phulusa la ngʼombeyo ayeneranso kuchapa zovala zake. Iyenso adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Ili likhale lamulo la nthawi zonse kwa Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo.

Onani mutuwo



Numeri 19:10
10 Mawu Ofanana  

Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m'dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakati pa inu.


ndipo aliyense akanyamulako nyama ya mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndiponso iye wakulowa m'nyumba masiku ake ili yotsekedwa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndi iye amene anazitentha atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, ndipo atatero alowenso kuchigono.


Ndipo woyerayo awaze pa wodetsedwayo tsiku lachitatu, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri amyeretse; ndipo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala woyera madzulo.


Ndipo likhale kwa iwo lemba losatha; kuti iye wakuwaza madzi akusiyanitsa azitsuka zovala zake; ndi iye wakukhudza madzi akusiyanitsa adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Msukuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse.