Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka chifukwa cha dziko, ndi mliri wa pa Israele unalekeka.
Numeri 16:48 - Buku Lopatulika Ndipo anaima pakati pa akufa ndi amoyo; ndi mliri unaleka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anaima pakati pa akufa ndi amoyo; ndi mliri unaleka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aroni adakaima pakati pa anthu akufa ndi amoyo aja, ndipo mliriwo udaleka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayimirira pakati pa anthu amoyo ndi akufa ndipo mliri unaleka. |
Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka chifukwa cha dziko, ndi mliri wa pa Israele unalekeka.
Potero munthu yense anatenga mbale yake yofukizamo, naikamo moto, naikapo chofukiza, naima pa khomo la chihema chokomanako pamodzi ndi Mose ndi Aroni.
Ndipo moto unatuluka kwa Yehova, ndi kunyeketsa amuna mazana awiri ndi makumi asanu aja akubwera nacho chofukiza.
Ndipo Aroni anatenga monga Mose adanena, nathamanga kulowa pakati pa msonkhano; ndipo taonani, udayamba mliri pakati pa anthu; ndipo anaikapo chofukiza nawachitira anthu chowatetezera.
Koma akufa nao mliri ndiwo zikwi khumi ndi zinai mphambu mazana asanu ndi awiri, osawerenga aja adafera chija cha Kora.
Zitapita izi Yesu anampeza mu Kachisi, nati kwa iye, Taona, wachiritsidwa; usachimwenso, kuti chingakugwere choipa choposa.
ndi kulindirira Mwana wake achokere Kumwamba, amene anamuukitsa kwa akufa, Yesu, wotipulumutsa ife kumkwiyo ulinkudza.
Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.