Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 5:14 - Buku Lopatulika

14 Zitapita izi Yesu anampeza mu Kachisi, nati kwa iye, Taona, wachiritsidwa; usachimwenso, kuti chingakugwere choipa choposa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Zitapita izi Yesu anampeza m'Kachisi, nati kwa iye, Taona, wachiritsidwa; usachimwenso, kuti chingakugwere choipa choposa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Pambuyo pake Yesu adapeza wochira uja m'Nyumba ya Mulungu, namuuza kuti, “Ona, wachira tsopano. Usakachimwenso, kuti chingakugwere choopsa china kuposa pamenepa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Patapita nthawi Yesu anamupeza ku Nyumba ya Mulungu ndipo anati kwa iye, “Taona uli bwino tsopano. Usakachimwenso kuti choyipa choposa ichi chingakugwere.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 5:14
23 Mawu Ofanana  

Ndipo nthawi ya nsautso yake anaonjeza kulakwira Yehova, mfumu Ahazi yemweyo.


Koma atapumula, anabwereza kuchita choipa pamaso panu; chifukwa chake munawasiya m'dzanja la adani ao amene anachita ufumu pa iwo; koma pobwera iwo ndi kufuula kwa Inu, munamva mu Mwamba ndi kuwapulumutsa kawirikawiri, monga mwa chifundo chanu;


Kulanga anandilangadi Yehova: koma sanandipereke kuimfa ai.


Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga, ndipo malemba ake sindinawachotse kwa ine.


Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani anga akundizinga; ndipo ndidzapereka m'chihema mwake nsembe za kufuula mokondwera; ndidzaimba, inde, ndidzaimbira Yehova zomlemekeza.


Ndichitireni chifundo, Yehova; penyani kuzunzika kwanga kumene andichitira ondidawo, inu wondinyamula kundichotsa kuzipata za imfa.


Yehova ndiye wondipulumutsa ine; Chifukwa chake tidzaimba nyimbo zanga, ndi zoimba zazingwe Masiku onse a moyo wathu m'nyumba ya Yehova.


Hezekiya anatinso, Chizindikiro nchiyani, kuti ndidzakwera kunka kunyumba ya Yehova?


ndipo taonani, ngati chioneka chakumba kubzola khungu, ndipo tsitsi lake lisanduka lotuwa, pamenepo wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo nthenda yakhate yabuka m'chilondamo.


Ndipo mukapanda kundimvera Ine, chingakhale ichi, ndi kuyenda motsutsana nane;


akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, timitanda topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tootcha, ta ufa wosalala tosakaniza ndi mafuta.


Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu ina inzake isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ake. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.


Ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, machimo ako akhululukidwa.


Koma wochiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani; pakuti Yesu anachoka kachetechete, popeza panali anthu aunyinji m'malo muja.


Koma panali munthu wina apo, ali m'kudwala kwake zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu.


Koma iye anati, Palibe, Ambuye. Ndipo Yesu anati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usachimwenso.


Pakuti nthawi yapitayi idakufikirani kuchita chifuniro cha amitundu, poyendayenda inu m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa