Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 5:15 - Buku Lopatulika

15 Munthuyo anachoka, nauza Ayuda, kuti ndiye Yesu amene adamchiritsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Munthuyo anachoka, nauza Ayuda, kuti ndiye Yesu amene adamchiritsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Munthuyo adapita nakauza Ayuda kuti Yesu ndiye amene wamchiritsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Munthu uja anachoka ndi kukawawuza Ayuda kuti anali Yesu amene anamuchiritsa iye.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 5:15
12 Mawu Ofanana  

Koma iye anatuluka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanathe kulowanso poyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a kumalo onse.


Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?


Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga?


Chifukwa chake Ayuda ananena kwa wochiritsidwayo, Ndi Sabata, ndipo sikuloledwa kwa iwe kuyalula mphasa yako.


Anamfunsa, Munthuyo ndani wonena ndi iwe, Yalula mphasa yako, nuyende?


Ndipo chifukwa cha ichi Ayuda analondalonda Yesu, popeza anachita izo tsiku la Sabata.


Chifukwa cha ichi Ayuda anaonjeza kufuna kumupha, si chifukwa cha kuswa tsiku la Sabata kokha, komatu amatchanso Mulungu Atate wake wa Iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.


Pamenepo ndipo Afarisi anamfunsanso, umo anapenyera. Ndipo anati kwa iwo, Anapaka thope m'maso mwanga, ndinasamba, ndipo ndipenya.


Pamenepo iyeyu anayankha, Ngati ali wochimwa, sindidziwa; chinthu chimodzi ndichidziwa, pokhala ndinali wosaona, tsopano ndipenya.


Munthuyu anayankha nati kwa iwo, Pakuti chozizwa chili m'menemo, kuti inu simudziwa kumene achokera, ndipo ananditsegulira maso anga.


Anayankha nati kwa iye, Wabadwa iwe konse m'zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo anamtaya kunja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa