Numeri 15:40 - Buku Lopatulika kuti mukumbukire ndi kuchita malamulo anga onse, ndi kukhala wopatulikira Mulungu wanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti mukumbukire ndi kuchita malamulo anga onse, ndi kukhala wopatulikira Mulungu wanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho mudzakumbukira ndi kugwiritsa ntchito malamulo anga onse, mudzakhala oyera mtima pamaso pa Mulungu wanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Motero mudzakumbukira kumvera malamulo anga ndipo mudzakhala opatulikira a Mulungu wanu. |
Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, nuti nao, Muzikhala oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.
Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakukutulutsani m'dziko la Ejipito, kuti ndikhale Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chilema pamaso pake m'chikondi.
kwa oyera mtima ndi abale okhulupirika mwa Khristu a mu Kolose: Chisomo kwa inu ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu.