Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 15:39 - Buku Lopatulika

39 Ndipo chikhale kwa inu mphonje, yakuti muziyang'anirako, ndi kukumbukira malamulo onse a Yehova, ndi kuwachita, ndi kuti musamazondazonda kutsata za m'mtima mwanu, ndi za m'maso mwanu zimene mumatsata ndi chigololo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Ndipo chikhale kwa inu mphonje, yakuti muziyang'anirako, ndi kukumbukira malamulo onse a Yehova, ndi kuwachita, ndi kuti musamazondazonda kutsata za m'mtima mwanu, ndi za m'maso mwanu zimene mumatsata ndi chigololo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Mphonje imeneyo muzidzaiyang'ana ndi kumakumbukira malamulo onse a Chauta, kuti muziŵamvera, ndipo musamatsatenso zilakolako zokhota za mtima wanu kapena za maso anu zimene munkazitsata.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Mudzakhala ndi mphonje zimenezi kuti mukaziona muzikakumbukira malamulo onse a Yehova ndi kuwamvera kuti musamatsatenso zilakolako za mʼmitima mwanu ndi za maso anu.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 15:39
21 Mawu Ofanana  

Ndipo anapereka nsembe paguwa la nsembe analimanga mu Betele, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chitatu, m'mwezi umene anaulingirira m'mtima mwa iye yekha, nawaikira ana a Israele madyerero, napereka nsembe paguwa la nsembe, nafukiza zonunkhira.


Ngati phazi langa linapatuka m'njira, ndi mtima wanga unatsata maso anga? Ngati chilema chamamatira manja anga?


Ndipo anadziipsa nazo ntchito zao, nachita chigololo nao machitidwe ao.


Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzaonongeka; muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu.


Ndipo chizikhala ndi iwe ngati chizindikiro padzanja lako, ndi chikumbutso pakati pamaso ako; kuti chilamulo cha Yehova chikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakutulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.


Wokhulupirira mtima wakewake ali wopusa; koma woyenda mwanzeru adzapulumuka.


Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga;


Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m'njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.


koma anatsata kuuma kwa mtima wao, ndi Baala, monga makolo ao anawaphunzitsa;


Pamenepo akupulumuka anu adzandikumbukira Ine kwa amitundu kumene anatengedwa ndende, kuti ndasweka ndi mtima wao wachigololo wolekana ndi Ine, ndi maso ao achigololo akutsata mafano ao; ndipo iwo adzakhala onyansa pamaso pao pa iwo eni, chifukwa cha zoipa anazichita m'zonyansa zao zonse.


Mutsutsane naye mai wanu, mutsutsane naye; pakuti sali mkazi wanga, ndi Ine sindili mwamuna wake; ndipo achotse zadama zake pankhope pake, ndi zigololo zake pakati pa mawere ake;


Ndipo kungakhale, akamva mau a lumbiro ili adzadzidalitsa m'mtima mwake, ndi kuti, Ndidzakhala nao mtendere, ndingakhale ndiyenda nao mtima wanga wopulukira, kuledzera nditamva ludzu;


Dzichenjerani, mungaiwale chipangano cha Yehova Mulungu wanu, chimene anapangana nanu, ndi kuti mungadzipangire fano losema, chifaniziro cha kanthu kalikonse Yehova Mulungu wanu anakuletsani.


pamenepo mudzichenjera mungaiwale Yehova, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya ukapolo.


Chenjerani mungaiwale Yehova Mulungu wanu, ndi kusasunga malamulo ake, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero lino;


mtima wanu ungatukumuke, nimungaiwale Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya ukapolo;


Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa