Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israele, nafulumiza Davide pa iwo, nati, Muka, nuwerenge Israele ndi Yuda.
Numeri 14:12 - Buku Lopatulika Ndidzawakantha ndi mliri, ndi kuwachotsera cholowa chao, ndipo ndidzakusandutsa iwe mtundu wa anthu waukulu ndi wamphamvu koposa iwowa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidzawakantha ndi mliri, ndi kuwachotsera cholowa chao, ndipo ndidzakusandutsa iwe mtundu wa anthu waukulu ndi wamphamvu koposa iwowa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzaŵapha ndi mliri ndi kuŵalanda choloŵa chao, ndipo iwe ndidzakusandutsa mtundu waukulu ndi wamphamvu kupambana iwoŵa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzawakantha ndi mliri ndi kuwawononga. Koma ndidzakusandutsa iwe mtundu waukulu ndi wamphamvu kuposa iwo.” |
Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israele, nafulumiza Davide pa iwo, nati, Muka, nuwerenge Israele ndi Yuda.
ndipo tsopano ndileke, kuti ndipse mtima pa awo ndi kuwatha, ndi kukuza iwe ukhale mtundu waukulu.
Ndipo iwo anati, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; timuketu ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kumphera nsembe Yehova Mulungu wathu; kuti angatikanthe ndi mliri, kapena ndi lupanga.
Koma nyumba ya Israele inapandukira Ine m'chipululu, sanayende m'malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m'chipululu kuwatha.
Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakuchita chilango cha chipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m'mizinda mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m'manja mwa mdani.
Yehova adzakumamatiritsani mliri, kufikira akakuthani kukuchotsani kudziko, kumene mupitako kulilandira.