Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 26:25 - Buku Lopatulika

25 Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakuchita chilango cha chipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m'mizinda mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m'manja mwa mdani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakuchita chilango cha chipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m'midzi mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m'manja mwa mdani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Ndidzabweretsa lupanga pa inu limene lidzakulangani chifukwa chophwanya chipangano changa. Ndipo mukasonkhana m'mizinda mwanu, ndidzatumiza miliri pakati panu ndipo ndidzakuperekani m'manja mwa adani anu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Ndipo ndidzabweretsa lupanga pa inu ndi kukulangani chifukwa chophwanya pangano langa. Mukadzasonkhana mʼmizinda yanu, ndidzatumiza miliri pakati panu ndipo ndidzakuperekani mʼmanja mwa adani anu.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 26:25
42 Mawu Ofanana  

Chomwecho Yehova anatumiza mliri pa Israele kuyambira m'mawa kufikira nthawi yoikika; ndipo anafapo anthu zikwi makumi asanu ndi awiri kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.


Ndipo anthu anu Aisraele akawakantha adani ao chifukwa cha kuchimwira Inu, ndipo akabweranso kwa Inu, ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedza Inu m'nyumba muno;


M'dziko mukakhala njala, mukakhala mliri, mlaza, chinoni, dzombe, kapena kapuchi, adani ao akawamangira misasa m'dziko la mizinda yao, mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda;


Anamkwerera Salimanezere mfumu ya Asiriya kumthira nkhondo; ndipo Hoseya anamgonjera, namsonkhera mitulo.


Pakuti khamu la nkhondo la Aaramu linadza la anthu owerengeka; ndipo Yehova anapereka khamu lalikulu m'dzanja lao; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao. Motero anachitira Yowasi zomlanga.


Mulungu wakubwezera chilango, Yehova, Mulungu wakubwezera chilango, muoneke wowala.


Ndipo iwo anati, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; timuketu ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kumphera nsembe Yehova Mulungu wathu; kuti angatikanthe ndi mliri, kapena ndi lupanga.


koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; chifukwa m'kamwa mwa Yehova mwatero.


ndidzasankhiratu inu kulupanga, ndipo inu nonse mudzagwada ndi kuphedwa; pakuti pamene ndinaitana, inu simunayankhe; pamene ndinanena, simunamve; koma munachita choipa m'maso mwanga, ndi kusankha chimene Ine sindinakondwere nacho.


Ndipo ndidzataya uphungu wa Yuda ndi wa Yerusalemu m'malo ano; ndipo ndidzagwetsa iwo ndi lupanga pamaso pa adani ao, ndi padzanja la iwo amene afuna moyo wao; mitembo yao ndidzapatsa ikhale chakudya cha mbalame za m'mlengalenga, ndi cha zilombo za dziko lapansi.


Ndipo ndidzatuma lupanga, ndi njala, ndi mliri mwa iwo, mpaka athedwa m'dziko limene ndinapatsa iwo ndi makolo ao.


Mau a iwo akuthawa akupulumuka m'dziko la Babiloni, kuti alalikire mu Ziyoni kubwezera chilango kwa Yehova Mulungu wathu, kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.


Nolani mivi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; chifukwa alingalirira Babiloni kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.


Ndidzawabalalitsanso mwa amitundu, amene iwo kapena makolo ao sanawadziwe; ndipo ndidzatumiza lupanga, liwatsate mpaka ndawatha.


Wamng'ono ndi nkhalamba agona pansi m'makwalala; anamwali ndi anyamata anga agwa ndi lupanga; munawapha tsiku la mkwiyo wanu, munawagwaza osachitira chisoni.


Kapena ndikadza padziko ndi lupanga, ndi kuti, Lupanga lipite pakati padziko, kuti ndilidulire munthu ndi nyama;


Ndipo ndidzakupititsani pansi pa ndodo ya mbusa ndi kukulowetsani m'chimango cha chipangano;


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona, ndikudzera ndi lupanga, ndi kukulikhira munthu ndi nyama.


Wobadwa ndi munthu iwe, Nena ndi ana a anthu a mtundu wako, uziti nao, Ndikafikitsira dziko lililonse lupanga, nakatenga eni dziko munthu wa pakati pao, nakamuika awadikirire,


Inde ndidzakutumizirani njala ndi zilombo, ndipo zidzakusowetsa ana ako; ndi mliri ndi mwazi zidzakugwera; ndidzakufikitsiranso lupanga; Ine Yehova ndachinena.


nunene, Mapiri a Israele inu, tamverani mau a Yehova Mulungu: Atero Yehova Mulungu kwa mapiri ndi zitunda, kwa mitsinje ndi zigwa, Taonani, Ine ndikufikitsirani lupanga, ndipo ndidzaononga misanje yanu.


Ndi lupanga lidzagwera mizinda yake, lidzatha mipiringidzo yake, ndi kuononga chifukwa cha uphungu wao.


Ndipo ndidzapatsa mtendere m'dzikomo, kuti mudzagone pansi, wopanda wina wakukuopsani; ndidzaletsanso zilombo zisakhale m'dzikomo, lupanga lomwe silidzapita m'dziko mwanu.


Ndinatumiza mliri pakati panu monga mu Ejipito; anyamata anu ndawapha ndi lupanga, ndi kutenga akavalo anu; ndipo ndinakweretsa kununkha kwa chigono chanu kufikitsa kumphuno kwanu; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Patsogolo pake panapita mliri, ndi makala amoto anatuluka pa mapazi ake.


Ndidzawakantha ndi mliri, ndi kuwachotsera cholowa chao, ndipo ndidzakusandutsa iwe mtundu wa anthu waukulu ndi wamphamvu koposa iwowa.


Koma akufa nao mliri ndiwo zikwi khumi ndi zinai mphambu mazana asanu ndi awiri, osawerenga aja adafera chija cha Kora.


Ndipo Mose ananena ndi anthu, nati, Adzikonzere ena mwa inu zida za nkhondo, alimbane nao Amidiyani, kuwabwezera Amidiyani chilango cha Yehova.


ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m'malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zoopsa ndi zizindikiro zazikulu zakumwamba.


Yehova adzakumamatiritsani mliri, kufikira akakuthani kukuchotsani kudziko, kumene mupitako kulilandira.


Pabwalo lupanga lidzalanda, ndi m'zipinda mantha; lidzaononga mnyamata ndi namwali, woyamwa pamodzi ndi munthu waimvi.


Kubwezera chilango nkwanga, kubwezera komwe, pa nyengo ya kuterereka phazi lao; pakuti tsiku la tsoka lao layandika, ndi zinthu zowakonzeratu zifulumira kudza.


ndikanola lupanga langa lonyezimira, ndi dzanja langa likagwira chiweruzo; ndidzabwezera chilango ondiukira, ndi kulanga ondida.


Pamenepo anatsikira ku phanga la Etamu amuna zikwi zitatu a ku Yuda, nati kwa Samisoni, Sudziwa kodi kuti Afilisti ndiwo akutilamulira ife? Nchiyani ichi watichitira? Nati iye kwa iwowa, Monga anandichitira ine ndawachitira iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa