Iye analankhula nao mu mtambo woti njo: Iwo anasunga mboni zake ndi malembawa anawapatsa.
Numeri 12:5 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anatsika mumtambo njo, naima pa khomo la chihema, naitana Aroni ndi Miriyamu; natuluka onse awiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anatsika mumtambo njo, naima pa khomo la chihema, naitana Aroni ndi Miriyamu; natuluka onse awiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adatsika mu mtambo, naima pakhomo pa hema, ndipo adaitana Aroni ndi Miriyamu, tsono aŵiri onsewo adabweradi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Yehova anatsika mu mtambo, nayima pa khomo la chihema. Kenaka anayitana Aaroni ndi Miriamu. Ndipo onse awiri atapita patsogolo, |
Iye analankhula nao mu mtambo woti njo: Iwo anasunga mboni zake ndi malembawa anawapatsa.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akuvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo.
Pakuti mtambo wa Yehova unakhala pa chihema msana, ndi usiku munali moto m'menemo, pamaso pa mbumba yonse ya Israele, m'maulendo ao onse.
Ndipo Yehova anatsika mumtambo, nanena naye, natengako mzimu uli pa iye, nauika pa akulu makumi asanu ndi awiri; ndipo kunali kuti pokhala mzimu pa iwowa, ananenera; koma osabwerezanso.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, ndi Aroni, ndi Miriyamu modzidzimutsa, Tulukani inu atatu kudza ku chihema chokomanako. Pamenepo anatuluka atatuwo.