Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
Numeri 12:15 - Buku Lopatulika Pamenepo anambindikiritsa Miriyamu kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo anthu sanayende ulendo kufikira atamlandiranso Miriyamu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo anambindikiritsa Miriyamu kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo anthu sanayende ulendo kufikira atamlandiranso Miriyamu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho adamtsekera Miriyamu kunja kwa mahema masiku asanu ndi aŵiri. Ndipo anthu sadathe kunyamuka ulendo wao mpaka Miriyamu atamloŵetsanso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anamutsekera Miriamu kunja kwa msasa masiku asanu ndi awiri ndipo anthu sanayende ulendo wawo mpaka Miriamu atamulowetsanso. |
Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
Ndipo iye wakuti ayeretsedwe atsuke zovala zake, namete tsitsi lake lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kuchigono, koma agone pa bwalo la hema wake masiku asanu ndi awiri.
Pakuti ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriyamu.
Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha; Yehova, tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka, pakati pa zaka mudziwitse; pa mkwiyo mukumbukire chifundo.
Ndipo atatero anthuwo ananka ulendo wao kuchokera ku Hazeroti, namanga mahema ao m'chipululu cha Parani.