Numeri 11:7 - Buku Lopatulika Ndipo mana ananga zipatso zampasa, ndi maonekedwe ake ngati maonekedwe a bedola. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mana ananga zipatso zampasa, ndi maonekedwe ake ngati maonekedwe a bedola. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Manayo ankafanafana ndi njere za mapira, ndipo maonekedwe ake anali ngati ulimbo wouma. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mana ankafanana ndi mbewu zamapira ndipo maonekedwe ake anali ngati ulimbo wowuma. |
Ndipo ananena nao, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; chimene muziotcha, otchani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m'mawa.
Ndipo mbumba ya Israele inautcha dzina lake Mana; ndiwo ngati zipatso zampasa, oyera; powalawa akunga timitanda tosakaniza ndi uchi.
Anthu amanka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta.
Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wopambana, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pamwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu aliyense koma iye wakuulandira.