Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 11:5 - Buku Lopatulika

Tikumbukira nsomba tinazidya mu Ejipito chabe, minkhaka, ndi mavwende, ndi anyezi wa mitundu itatu;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Tikumbukira nsomba tinazidya m'Ejipito chabe, minkhaka, ndi mavwende, ndi anyezi a mitundu itatu;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinkadya ku Ejipito, minkhaka ija, mavwende ndi anyezi wamitundu-mitundu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinkadya ku Igupto komanso nkhaka, mavwende, anyezi wamitundumitundu ndi adyo.

Onani mutuwo



Numeri 11:5
7 Mawu Ofanana  

kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.


nanena nao ana a Israele, Ha? Mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Ejipito, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife chokhuta; pakuti mwatitulutsa kudza nafe m'chipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.


Ndipo mwana wamkazi wa Ziyoni wasiyidwa ngati chitando cha m'munda wampesa, chilindo cha m'munda waminkhaka, ngati mzinda wozingidwa ndi nkhondo.


ndi kuti, Iai; tidzanka ku Ejipito, kumene sitidzaona nkhondo, sitidzamva kulira kwa lipenga, sitidzamva njala yokhumba mkate; pamenepo tidzakhala;


Koma chilekere ife kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, tasowa zonse, tathedwa ndi lupanga ndi njala.


Ndipo ana onse a Israele anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Ejipito; kapena mwenzi tikadafa m'chipululu muno!


chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko.