Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 11:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo anthu osokonezeka ali pakati pao anagwidwa nacho chilakolako; ndi ana a Israele omwe analiranso, nati, Adzatipatsa nyama ndani?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anthu osokonezeka ali pakati pao anagwidwa nacho chilakolako; ndi ana a Israele omwe analiranso, nati, Adzatipatsa nyama ndani?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Nthaŵi imeneyo anthu ena osokoneza amene anali pakati pa Aisraele adamva nkhuli yaikulu. Aisraelenso adayamba kudandaula, adati, “Ndani adzatipatsa nyama kuti tizidya?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Anthu ena osokoneza amene anali pakati pa Aisraeli anayamba kukhumba chakudya cha ku Igupto ndipo Aisraeli nawonso anayamba kufuwula kwambiri nʼkumati, “Tikanangopeza nyama yoti nʼkudya!

Onani mutuwo Koperani




Numeri 11:4
16 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, atamva chilamulocho, anasiyanitsa pa Israele anthu osokonezeka onse.


Popeza analakalakatu kuchidikhako, nayesa Mulungu m'chipululu.


Ndipo anthu ambiri osokonezeka anakwera nao; ndi nkhosa ndi ng'ombe, zoweta zambirimbiri.


Ndamva madandaulo a ana a Israele; lankhula nao ndi kuti, Madzulo mudzadya nyama, ndi m'mawa mudzakhuta mkate; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


nanena nao ana a Israele, Ha? Mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Ejipito, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife chokhuta; pakuti mwatitulutsa kudza nafe m'chipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.


ndi kuti, Iai; tidzanka ku Ejipito, kumene sitidzaona nkhondo, sitidzamva kulira kwa lipenga, sitidzamva njala yokhumba mkate; pamenepo tidzakhala;


Ndipo unene ndi anthu, Mudzipatuliretu, mawa mudzadya nyama; popeza mwalira m'makutu a Yehova, ndi kuti, Adzatipatsa nyama ndani? Popeza tinakhala bwino mu Ejipito. Potero Yehova adzakupatsani nyama, ndipo mudzadya.


Pamenepo khamu lonse linakweza mau ao, nafuula; ndipo anthuwo analira usikuwo.


popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita mu Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;


kodi ndi chinthu chaching'ono kuti watikweza kutichotsa m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, kutipha m'chipululu; koma udziyesanso ndithu kalonga wa ife?


Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.


Koma zinthu izi zinachitika, zikhale zotichenjeza ife, kuti tisalakalake zoipa ife, monganso iwowo analakalaka.


Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.


Ku Tabera, ndi ku Masa, ndi ku Kibroti-Hatava, munautsanso mkwiyo wa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa