Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 11:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinkadya ku Igupto komanso nkhaka, mavwende, anyezi wamitundumitundu ndi adyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 Tikumbukira nsomba tinazidya mu Ejipito chabe, minkhaka, ndi mavwende, ndi anyezi wa mitundu itatu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Tikumbukira nsomba tinazidya m'Ejipito chabe, minkhaka, ndi mavwende, ndi anyezi a mitundu itatu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinkadya ku Ejipito, minkhaka ija, mavwende ndi anyezi wamitundu-mitundu.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 11:5
7 Mawu Ofanana  

Inu Yehova, pulumutseni ndi dzanja lanu kwa anthu otere, kwa anthu a dziko lino amene mphotho yawo ili mʼmoyo uno. Inu mumaletsa njala kwa amene asangalatsidwa nanu; ana awo aamuna ali ndi zinthu zambiri, ndipo iwo amasunga chuma cha ana awo.


kuti, “Kukanakhala bwino Yehova akanatiphera mʼdziko la Igupto! Kumeneko timadya nyama ndi buledi mpaka kukhuta, koma inu mwabwera nafe ku chipululu kudzapha mpingo wonsewu ndi njala!”


Mwana wamkazi wa Ziyoni watsala yekha ngati nsanja mʼmunda wampesa, ngati chisimba mʼmunda wa minkhaka, ngati mzinda wozingidwa ndi nkhondo.


ndipo ngati mukunena kuti, ‘Ayi, koma tidzapita ku Igupto kumene sitidzaonako nkhondo kapena kumva kulira kwa lipenga kapenanso kusowa chakudya.’


Koma kuchokera nthawi imene tinasiya kufukiza lubani ndi kupereka chopereka cha chakumwa kwa mfumukazi yakumwamba, ifeyo takhala tikusowa zinthu ndipo takhala tikuphedwa ndi lupanga ndi kufa ndi njala.”


Ndipo Aisraeli onse anayankhula motsutsana ndi Mose ndi Aaroni. Gulu lonse linanena kwa iwo kuti, “Kunali bwino tikanafera ku Igupto kapena mʼchipululu muno!


Mapeto awo ndi chiwonongeko, mulungu wawo ndi mimba zawo, ndipo ulemerero wawo ndi manyazi awo. Mtima wawo uli pa zinthu za dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa