Pamenepo munalankhula m'masomphenya ndi okondedwa anu, ndipo mudati, Ndasenza thandizo pa chiphona; ndakweza wina wosankhika mwa anthu.
Numeri 11:14 - Buku Lopatulika Sinditha kuwasenza anthu awa onse ndekha, pakuti andilemera ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sinditha kuwasenza anthu awa onse ndekha, pakuti andilemera ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ine sindingathe kuŵasamala ndekha anthu onseŵa. Katundu ameneyu sindingathe kumsenza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sindingathe kusamala anthu onsewa ndekha. Katundu ameneyu ndi wolemera kwambiri kwa ine. |
Pamenepo munalankhula m'masomphenya ndi okondedwa anu, ndipo mudati, Ndasenza thandizo pa chiphona; ndakweza wina wosankhika mwa anthu.
Udzalema konse, iwe ndi anthu amene uli nao; pakuti chikukanika chinthu ichi; sungathe kuchichita pa wekha.
Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.
inde adzamanga Kachisi wa Yehova; nadzasenza ulemererowo, nadzakhala ndi kulamulira pa mpando wachifumu wake; nadzakhala wansembe pampando wachifumu wake; ndi uphungu wa mtendere udzakhala pakati pa iwo awiri.