Fuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga cholakwa chao, ndi banja la Yakobo machimo ao.
Numeri 10:5 - Buku Lopatulika Mukaliza chokweza ayende a m'zigono za kum'mawa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mukaliza chokweza ayende a m'zigono za kum'mawa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mukaliza lipenga lochenjeza, anthu a m'mahema akuvuma ayambepo ulendo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akaliza lipenga lochenjeza, misasa yomwe ili kummawa iyambe kusamuka. |
Fuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga cholakwa chao, ndi banja la Yakobo machimo ao.
Muombe lipenga mu Ziyoni, nimufuulitse m'phiri langa lopatulika; onse okhala m'dziko anjenjemere; pakuti tsiku la Yehova lilinkudza, pakuti liyandikira;
Ndipo anayamba kuyenda ambendera ya chigono cha ana a Yuda monga mwa magulu ao; woyang'anira gulu lake ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.