Munawatsogoleranso usana ndi mtambo woti njo, ndi moto tolo usiku, kuwaunikira m'njira akayendamo.
Numeri 10:34 - Buku Lopatulika Ndipo mtambo wa Yehova unali pamwamba pao msana, pakuyenda iwo kuchokera kuchigono. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mtambo wa Yehova unali pamwamba pao msana, pakuyenda iwo kuchokera kuchigono. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtambo wa Chauta unkaŵaphimba masana, nthaŵi iliyonse pamene ankanyamuka pamahemapo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtambo wa Yehova unkawaphimba masana pamene ankasamuka pa misasa yawo. |
Munawatsogoleranso usana ndi mtambo woti njo, ndi moto tolo usiku, kuwaunikira m'njira akayendamo.
koma Inu mwa nsoni zanu zazikulu simunawasiye m'chipululu; mtambo woti njo sunawachokere usana kuwatsogolera m'njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo.
Pakuti mtambo wa Yehova unakhala pa chihema msana, ndi usiku munali moto m'menemo, pamaso pa mbumba yonse ya Israele, m'maulendo ao onse.
Ndipo kunali pakuchokera kunka nalo likasa, Mose anati, Ukani Yehova, abalalike adani anu; akuda Inu athawe pamaso panu.