Nenani mu Yuda, lalikirani mu Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m'dzikomo; fuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m'mizinda ya malinga.
Numeri 10:3 - Buku Lopatulika Akaliza, khamu lonse lisonkhane kuli iwe ku khomo la chihema chokomanako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akaliza, khamu lonse lisonkhane kuli iwe ku khomo la chihema chokomanako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akaliza aŵiri onsewo, mpingo wonse usonkhane kwa iwe pa chipata cha chihema chamsonkhano. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene akuliza malipenga onse awiri, anthu onse asonkhane kwa iwe pa khomo la tenti ya msonkhano. |
Nenani mu Yuda, lalikirani mu Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m'dzikomo; fuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m'mizinda ya malinga.
Muombe lipenga mu Ziyoni, nimufuulitse m'phiri langa lopatulika; onse okhala m'dziko anjenjemere; pakuti tsiku la Yehova lilinkudza, pakuti liyandikira;