Pakuti simudzachoka mofulumira, kapena kunka mothawa; pakuti Yehova adzakutsogolerani, ndi Mulungu wa Israele adzadikira pambuyo panu.
Numeri 10:25 - Buku Lopatulika Pamenepo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Ahiyezere mwana wa Amisadai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Ahiyezere mwana wa Amisadai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Potsiriza otsata mbendera ya zithando za Adani amene anali kumbuyo kwa anthu a mahema onse, adanyamuka m'magulumagulu, ndipo mtsogoleri wa gulu lao anali Ahiyezere mwana wa Amishadai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pambuyo pa magulu onse panali magulu a msasa wa Dani, omwe ankateteza magulu onsewa ndipo ananyamuka potsatira mbendera yawo. Mtsogoleri wawo anali Ahiyezeri mwana wa Amisadai. |
Pakuti simudzachoka mofulumira, kapena kunka mothawa; pakuti Yehova adzakutsogolerani, ndi Mulungu wa Israele adzadikira pambuyo panu.
Pomwepo kuunika kwako kudzawalitsa monga m'mawa, ndi kuchira kwako kudzaonekera msangamsanga; ndipo chilungamo chako chidzakutsogolera; ulemerero wa Yehova udzakhala wotchinjiriza pambuyo pako.
Ndipo ansembe asanu ndi awiri, akunyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo ndi kutsogolera nazo likasa la Yehova, anayenda chiyendere naliza mphalasazo; ndi okonzeka kunkhondowo anawatsogolera, ndi akudza m'mbuyo anatsata likasa la Yehova, ansembe ali chiombere poyenda iwo.
Ndipo okonzeka kunkhondo anatsogolera ansembe akuliza mphalasa, koma akudza m'mbuyo anatsata likasa, ansembe ali chiombere poyenda iwo.