A ana a Nafutali, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Numeri 1:43 - Buku Lopatulika owerengedwa ao a fuko la Nafutali, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 owerengedwa ao a fuko la Nafutali, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Nafutali, adapezeka kuti ali 53,400. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Nafutali chinali 53,400. |
A ana a Nafutali, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Iwo ndiwo amene anawerengedwa, amene Mose anawerenga pamodzi ndi Aroni, ndi akalonga a Israele, ndiwo amuna khumi ndi awiri; yense kunenera nyumba ya kholo lake.
Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.
Iwo ndiwo mabanja a Nafutali, monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana anai.