Ulimbike mtima, ndipo tichite chamuna lero chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu; Yehova nachite chomkomera.
Nehemiya 4:8 - Buku Lopatulika napangana chiwembu iwo onse pamodzi, kudzathira nkhondo ku Yerusalemu, ndi kuchita chisokonezo m'menemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 napangana chiwembu iwo onse pamodzi, kudzathira nkhondo ku Yerusalemu, ndi kuchita chisokonezo m'menemo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adapangana za chiwembu choti akathire nkhondo Yerusalemu ndi kusokoneza anthu amumzindamo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono onse anapangana za chiwembu kuti abwere ndi kudzathira nkhondo anthu a ku Yerusalemu ndi kuyambitsa mapokoso pakati pawo. |
Ulimbike mtima, ndipo tichite chamuna lero chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu; Yehova nachite chomkomera.
Limbani, mulimbike mtima, musaopa kapena kutenga nkhawa pankhope pa mfumu ya Asiriya ndi aunyinji okhala naye; pakuti okhala nafe achuluka koposa okhala naye;
ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake;
Koma kunali, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Aarabu, ndi Aamoni, ndi Aasidodi, kuti makonzedwe a malinga a Yerusalemu anakula, ndi kuti mopasuka mwake munayamba kutsekeka, chidawaipira kwambiri;
Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.
Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto.