Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 4:7 - Buku Lopatulika

7 Koma kunali, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Aarabu, ndi Aamoni, ndi Aasidodi, kuti makonzedwe a malinga a Yerusalemu anakula, ndi kuti mopasuka mwake munayamba kutsekeka, chidawaipira kwambiri;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Koma kunali, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Aarabu, ndi Aamoni, ndi Aasidodi, kuti makonzedwe a malinga a Yerusalemu anakula, ndi kuti mopasuka mwake munayamba kutsekeka, chidawaipira kwambiri;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Koma pamene Sanibalati ndi Tobiya, ndiponso Arabu, Aamoni ndi Aasidodi adamva kuti ntchito yokonza makoma a Yerusalemu ikupita m'tsogolo, ndipo kuti malo ogamukagamuka aja akuŵakonzanso, adapsa mtima kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Koma pamene Sanibalati, Tobiya, Aarabu, Aamoni ndi anthu a ku Asidodi anamva kuti ntchito yokonzanso makoma a Yerusalemu ikupitirirabe ndipo kuti mipata ikutsekedwa, anapsa mtima kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 4:7
29 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.


Ndipo Yehova anamtumizira magulu a Ababiloni, ndi magulu a Aaramu, ndi magulu a Amowabu, ndi magulu a ana a Amoni, nawatumiza pa Yuda kuliononga, monga mwa mau a Yehova adawanena ndi dzanja la atumiki ake aneneriwo.


Ndipo zitatha izi, kunachitika kuti ana a Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi ena pamodzi ndi Aamoni, anadza kuyambana nkhondo ndi Yehosafati.


Adziwe mfumu kuti ife tinamuka kudziko la Yuda, kunyumba ya Mulungu wamkulu, yomangidwa ndi miyala yaikulu, ndi kuikidwa mitengo pamakoma, ndipo inachitika mofulumira ntchitoyi, ndipo inayenda bwino m'dzanja mwao.


Atamva Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapoloyo Mwamoni, chidawaipira kwakukulu, kuti wadza munthu kuwafunira ana a Israele chokoma.


Koma Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapolo Mwamoniyo, ndi Gesemu Mwarabu, anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Chiyani ichi muchichita? Mulikupandukira mfumu kodi?


Ndipo kunali, atamva Sanibalati kuti tinalikumanga lingali, kudamuipira, nakwiya kwakukulu, naseka Ayuda pwepwete.


Koma tinamanga lingali, ndi linga lonse linalumikizana kufikira pakatimpakati; popeza mitima ya anthu inalunjika kuntchito.


napangana chiwembu iwo onse pamodzi, kudzathira nkhondo ku Yerusalemu, ndi kuchita chisokonezo m'menemo.


Ndipo kunali atachimva adani athu onse, amitundu onse akutizinga anaopa, nagwadi nkhope; popeza anazindikira kuti ntchitoyi inachitika ndi Mulungu wathu.


ndi anthu onse osakanizidwa, ndi mafumu onse a dziko la Uzi, ndi mafumu onse a dziko la Afilisti, ndi Asikeloni, ndi Gaza, ndi Ekeroni, ndi otsala a Asidodi,


Ndipo Ismaele anatenga ndende otsala onse a anthu okhala mu Mizipa, ana aakazi a mfumu, ndi anthu onse amene anatsala mu Mizipa, amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anapatsira Gedaliya mwana wa Ahikamu; Ismaele mwana wa Netaniya anawatenga ndende, napita kukaolokera kwa ana a Amoni.


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za ana a Amoni, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatumbula akazi ali m'pakati a Giliyadi, kuti akuze malire ao;


ndipo ndidzalikha okhala mu Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yachifumu mu Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekeroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova.


Bukitsani kunyumba zachifumu za Asidodi, ndi kunyumba zachifumu za m'dziko la Ejipito, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero aakulu m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwake.


Koma m'mene anamva iwo analaswa mtima, nafuna kuwapha.


Ndipo chinjoka chinakwiya ndi mkazi, ndipo chinachoka kunka kuchita nkhondo ndi otsala a mbeu yake, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu.


Ndipo Nahasi Mwamoni ananena nao, Ndidzapangana nanu, ngati mulola kuti maso a ku dzanja lamanja anu onse akolowoledwe; potero ndidzanyazitsa Aisraele onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa