Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.
Mateyu 7:16 - Buku Lopatulika Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mudzawazindikira iwo ndi zipatso zawo. Kodi anthu amathyola mpesa pa mtengo wa minga, kapena nkhuyu pa nthula? |
Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.
Ukakoma mtengo, chipatso chake chomwe chikoma; ukaipa mtengo, chipatso chake chomwe chiipa; pakuti ndi chipatso chake mtengo udziwika.
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,
Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiriro, ndipo ine ndili nazo ntchito; undionetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m'ntchito zanga.
Kodi mkuyu ukhoza kubala azitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sangathe kutulutsa okoma.
Monga umanena mwambi wa makolo, kuti, Uchimo utulukira mwa ochimwa; koma dzanja langa silidzakhala pa inu.