Ndipo pakutuluka pao anapeza munthu wa ku Kirene, dzina lake Simoni, namkakamiza iye kuti anyamule mtanda wake.
Mateyu 5:41 - Buku Lopatulika Ndipo amene akakukakamiza kumperekeza njira imodzi, upite naye ziwiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo amene akakukakamiza kumperekeza njira imodzi, upite naye ziwiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu akakukakamiza kuyenda naye mtunda umodzi, uyende naye mitunda iŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati wina akukakamiza kuti uyende naye mtunda umodzi, iwe uyende naye mitunda iwiri. |
Ndipo pakutuluka pao anapeza munthu wa ku Kirene, dzina lake Simoni, namkakamiza iye kuti anyamule mtanda wake.
Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso chofunda chako.
Ndipo anakakamiza wina wopitirirapo, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, atate wao wa Aleksandro ndi Rufu, kuti anyamule mtanda wake.
Ndipo popita naye, anagwira munthu, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pake pa Yesu.
Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa;