Marko 15:21 - Buku Lopatulika21 Ndipo anakakamiza wina wopitirirapo, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, atate wao wa Aleksandro ndi Rufu, kuti anyamule mtanda wake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201421 Ndipo anakakamiza wina wopitirirapo, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, atate wao wa Aleksandro ndi Rufu, kuti anyamule mtanda wake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa21 Pa njira adakumana ndi munthu wina, amene ankadutsa pamenepo kuchokera ku midzi. Munthuyo anali Simoni wa ku Kirene, bambo wake wa Aleksandro ndi Rufu. Tsono asilikali aja adamkakamiza kuti asenze mtanda wa Yesu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero21 Munthu wina ochokera ku Kurene, Simoni, abambo a Alekisanda ndi Rufasi amadutsa kuchokera ku dziko la kwawo, ndipo anamuwumiriza kuti anyamule mtanda. Onani mutuwo |