Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 23:26 - Buku Lopatulika

26 Ndipo popita naye, anagwira munthu, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pake pa Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipo popita naye, anagwira munthu, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pake pa Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Asilikali adamtenga Yesu napita naye kuti akampachike. Pa njira adagwira munthu wina wa ku Kirene, dzina lake Simoni. Iye ankachokera ku midzi. Adamsenzetsa mtanda wa Yesu kuti aunyamule, azitsatira pambuyo pa Yesuyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Ndipo pamene ankapita naye, anagwira Simoni wa ku Kurene, amene ankachokera ku munda, namusenzetsa mtanda namuyendetsa pambuyo pa Yesu.

Onani mutuwo Koperani




Luka 23:26
11 Mawu Ofanana  

Ndipo amene akakukakamiza kumperekeza njira imodzi, upite naye ziwiri.


Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake wa mwini yekha, ndi kudza pambuyo panga, sangathe kukhala wophunzira wanga.


Ndipo anawamasulira amene adaponyedwa m'ndende chifukwa cha mpanduko ndi kupha munthu, amene iwo anampempha; koma anapereka Yesu mwa chifuniro chao.


Ndipo Iye ananena kwa onse, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine.


Ndipo kunali aneneri ndi aphunzitsi ku Antiokeya mu Mpingo wa komweko, ndiwo Barnabasi, ndi Simeoni, wonenedwa Wakuda, ndi Lusio wa ku Kirene, Manaene woleredwa pamodzi ndi Herode chiwangacho, ndi Saulo.


mu Frijiya, ndiponso mu Pamfiliya, mu Ejipito, ndi mbali za Libiya wa ku Kirene, ndi alendo ochokera ku Roma,


amenewo anawaika pamaso pa atumwi; ndipo m'mene adapemphera, anaika manja pa iwo.


Koma anauka ena a iwo ochokera m'sunagoge wa Alibertino, ndi Akirene, ndi Aaleksandriya, ndi mwa iwo a ku Silisiya ndi ku Asiya, natsutsana ndi Stefano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa