Kodi simunamtchinge iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomzinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoweta zake zachuluka m'dziko.
Mateyu 4:6 - Buku Lopatulika nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti, Adzalamula angelo ake za iwe, ndipo pa manja ao adzakunyamula iwe, ungagunde konse phazi lako pamwala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti, Adzalamula angelo ake za iwe, ndipo pa manja ao adzakunyamula iwe, ungagunde konse phazi lako pamwala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adamuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, mudziponye pansi. Paja Malembo akuti, “ ‘Mulungu adzalamula angelo ake kuti akusamaleni, iwo adzakunyamulani m'manja mwao, kuti mapazi anu angapweteke pa miyala.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, dziponyeni nokha pansi. Pakuti kwalembedwa: “ ‘Adzalamulira angelo ake za iwe, ndipo adzakunyamula ndi manja awo kuti phazi lako lisagunde pa mwala.’ ” |
Kodi simunamtchinge iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomzinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoweta zake zachuluka m'dziko.
Pakuti udzakhala ndi pangano ndi miyala yakuthengo; ndi nyama zakuthengo zidzakhala nawe mumtendere.
Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akutuluka m'kamwa mwa Mulungu.
Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?