Pakuti Ine Yehova ndikonda chiweruziro, ndida chifwamba ndi choipa; ndipo ndidzawapatsa mphotho yao m'zoonadi; ndipo ndidzapangana nao pangano losatha.
Mateyu 27:6 - Buku Lopatulika Ndipo ansembe aakulu anatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziika m'chosonkhera ndalama za Mulungu, chifukwa ndizo mtengo wa mwazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ansembe aakulu anatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziika m'chosonkhera ndalama za Mulungu, chifukwa ndizo mtengo wa mwazi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akulu a ansembe aja adatola ndalamazo nati, “Malamulo athu satilola kuika ndalamazi m'bokosi la chuma cha m'Nyumba ya Mulungu, popeza kuti ndi za magazi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akulu a ansembe anatola ndalamazo nati, “Sikololedwa ndi lamulo kuti ndalamazi tiziyike mosungira chuma cha Mulungu, popeza ndi ndalama za magazi.” |
Pakuti Ine Yehova ndikonda chiweruziro, ndida chifwamba ndi choipa; ndipo ndidzawapatsa mphotho yao m'zoonadi; ndipo ndidzapangana nao pangano losatha.
koma inu munena, Munthu akati kwa atate wake, kapena amai wake, Korban, ndiko kuti Mtulo, chimene ukadathandizidwa nacho ndi ine,
Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowe ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska.
Musamabwera nayo mphotho ya wachigololo, kapena mtengo wake wa galu kulowa nazo m'nyumba ya Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha chowinda chilichonse; pakuti onse awiriwa Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.