Ndipo anaika manda ake pamodzi ndi oipa, ndi pamodzi ndi olemera mu imfa yake, ngakhale Iye sanachite chiwawa, ndipo m'kamwa mwake munalibe chinyengo.
Mateyu 27:57 - Buku Lopatulika Ndipo pamene panali madzulo, anadza munthu wachuma wa ku Arimatea, dzina lake Yosefe, amene analinso wophunzira wa Yesu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene panali madzulo, anadza munthu wachuma wa ku Arimatea, dzina lake Yosefe, amene analinso wophunzira wa Yesu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chisisira chitagwa, kudafika munthu wina wolemera, wochokera ku Arimatea, dzina lake Yosefe. Nayenso anali wophunzira wa Yesu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene kumada, kunabwera munthu wolemera wa ku Arimateyu dzina lake Yosefe amene anali wophunzira wa Yesu. |
Ndipo anaika manda ake pamodzi ndi oipa, ndi pamodzi ndi olemera mu imfa yake, ngakhale Iye sanachite chiwawa, ndipo m'kamwa mwake munalibe chinyengo.
yemweyo anapita kwa Pilato, napempha mtembo wa Yesu. Pomwepo Pilato analamula kuti uperekedwe.
Ndipo panali munthu wina wa ku Ramatayimu Zofimu, wa dziko la mapiri la Efuremu, dzina lake ndiye Elikana, mwana wake wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufu, Mwefuremu.
Ndipo anabwera ku Rama, pakuti nyumba yake inali kumeneko; ndipo pamenepo anaweruza Israele; namangapo guwa la nsembe la Yehova.