Nafulumira iwo, nagwira yense chofunda chake, nachiyala pokhala iye pachiunda, naomba lipenga, nati, Yehu ndiye mfumu.
Mateyu 21:8 - Buku Lopatulika Ndipo ambirimbiri a mpingowo anayala zovala zao panjira; ndipo ena anadula nthambi za mitengo, naziyala m'njiramo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ambirimbiri a mpingowo anayala zovala zao panjira; ndipo ena anadula nthambi za mitengo, naziyala m'njiramo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu ambiri ankayala zovala zao mu mseu, ndipo ena adakadula nthambi za mitengo nkumaziyalika mumseumo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Gulu lalikulu la anthu linayala zovala zawo mu msewu pamene ena anadula nthambi zamitengo ndi kuziyala mu msewumo. |
Nafulumira iwo, nagwira yense chofunda chake, nachiyala pokhala iye pachiunda, naomba lipenga, nati, Yehu ndiye mfumu.
Ndipo tsiku loyambali mudzitengere nthambi za mitengo yokoma, nsomo za kanjedza, ndi nthambi za mitengo yovalira, ndi misondodzi ya kumtsinje; ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu masiku asanu ndi awiri.
anatenga makwata a kanjedza, natuluka kukakomana ndi Iye, nafuula, Hosana; wolemekezeka Iye wakudza m'dzina la Ambuye, ndiye mfumu ya Israele.