Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 9:13 - Buku Lopatulika

13 Nafulumira iwo, nagwira yense chofunda chake, nachiyala pokhala iye pachiunda, naomba lipenga, nati, Yehu ndiye mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Nafulumira iwo, nagwira yense chofunda chake, nachiyala pokhala iye pachiunda, naomba lipenga, nati, Yehu ndiye mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Pomwepo aliyense mwa iwowo adatenga mwinjiro wake nauyala pa makwerero, kuti Yehu akhalepo, ndipo adaliza lipenga, nalengeza kuti, “Yehu ndiye mfumu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Atsogoleri aja mofulumira anatenga zofunda zawo naziyala pansi pa makwerero kuti Yehu akhalepo. Kenaka analiza lipenga, nafuwula kuti, “Yehu ndiye mfumu!”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 9:13
12 Mawu Ofanana  

Koma Abisalomu anatumiza ozonda ku mafuko onse a Israele, kuti, Pakumva kulira kwa lipenga, pomwepo muzinena, Abisalomu ali mfumu ku Hebroni.


Popeza iye watsika lero, nakapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana aamuna onse a mfumu, ndi akazembe a nkhondo, ndi Abiyatara wansembe; ndipo taonani, iwowo akudya ndi kumwa pamaso pake, nati, Akhale ndi moyo mfumu Adoniya.


Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri akamdzoze kumeneko akhale mfumu ya Israele; ndipo muombe lipenga, ndi kuti, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo.


Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali mu Chihema, namdzoza Solomoni. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo.


Atatero, anatulutsa mwana wa mfumu, namuika korona, nampatsa buku la umboni, namlonga ufumu, namdzoza, naomba m'manja, nati, Mfumu ikhale ndi moyo.


napenya, ndipo taonani, mfumu ili chilili pachiundo, monga ankachita, ndi atsogoleri ndi amalipenga pali mfumu; nakondwerera anthu onse a m'dziko, naomba malipenga. Pamenepo Ataliya anang'amba zovala zake, nafuula Chiwembu, Chiwembu.


Nati iwo, Kunama uku; utifotokozere tsono. Nati iye, Anati kwa ine chakutichakuti; ndi kuti, Atero Yehova, Ndakudzoza mfumu pa Israele.


Fuulani pamaso pa Mfumu Yehova, ndi mbetete ndi liu la lipenga.


Ndipo pakupita Iye, anayala zovala zao m'njira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa