Koma mtima wa mfumu ya Aramu unavutika kwambiri pa ichicho, naitana anyamata ake, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wovomerezana ndi mfumu ya Israele ndani?
Mateyu 2:3 - Buku Lopatulika Ndipo Herode mfumuyo pakumva ichi anavutika, ndi Yerusalemu yense pamodzi naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Herode mfumuyo pakumva ichi anavutika, ndi Yerusalemu yense pamodzi naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mfumu Herode atamva zimenezi, adavutika kwambiri ndipo anthu ena onse a m'Yerusalemu nawonso adavutika nazo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu Herode atamva zimenezi, anavutika mu mtima kwambiri pamodzi ndi anthu onse a mu Yerusalemu. |
Koma mtima wa mfumu ya Aramu unavutika kwambiri pa ichicho, naitana anyamata ake, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wovomerezana ndi mfumu ya Israele ndani?
nati, Ali kuti amene anabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.
Ndipo pamene anasonkhanitsa ansembe aakulu onse ndi alembi a anthu, anafunsira iwo, Adzabadwira kuti Khristuyo?
Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m'mapiko ake, koma inu simunafune ai!
Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma chitsiriziro sichinafike.
Ndipo onani, anafuula nati, Tili nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siinafike?
Ndipo m'mene mudzamva za nkhondo ndi mbiri zake za nkhondo, musamadera nkhawa: ziyenera kuchitika izi; koma sichinafike chimaliziro.