Mateyu 23:37 - Buku Lopatulika37 Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m'mapiko ake, koma inu simunafune ai! Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201437 Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m'mapiko ake, koma inu simunafuna ai! Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa37 “Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri, nkuŵaponya miyala anthu amene Mulungu amakutumizira. Nkangati ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa anthu ako, monga momwe nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake pansi pa mapiko ake, iwe nkumakana! Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero37 “Haa! Yerusalemu, Yerusalemu, iwe amene umapha aneneri ndi kugenda miyala amene atumidwa kwa iwe, kawirikawiri ndimafuna kusonkhanitsa ana ako, monga nkhuku imasonkhanitsira ana ake pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune. Onani mutuwo |
Chifukwa chanji ndinafika osapeza munthu? Ndi kuitana koma panalibe wina woyankha? Kodi dzanja langa lafupika konse, kuti silingathe kuombola? Pena Ine kodi ndilibe mphamvu zakupulumutsa? Taona pa kudzudzula kwanga ndiumitsa nyanja, ndi kusandutsa mitsinje chipululu; nsomba zake zinunkha chifukwa mulibe madzi, ndipo zifa ndi ludzu.